2 Mafumu 7:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Choncho akhate aja atafika ku malire a zithandozo, adakaloŵa mu hema limodzi, ndipo adadya ndi kumwa. Atatero adatengako siliva, golide ndi zovala, nakazibisa. Pambuyo pake adabwerera nakaloŵa mu hema linanso, natengamo zinthu, nkukazibisanso. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso. Onani mutuwo |