Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:7 - Buku Lopatulika

7 Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Motero adathaŵa ndi chisisila, nasiya mahema, akavalo, abulu ndiponso katundu wao yense monga momwe adaaliri, nathaŵa kuti apulumutse moyo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:7
18 Mawu Ofanana  

Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka mu Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.


Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.


Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake.


Kavalo safikana kupulumuka naye, chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa.


Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki, ndi mbalame kudzanja la msodzi.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


Ndipo anaima yense m'mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, nafuula, nathawa.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa