Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:6 - Buku Lopatulika

6 Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chauta anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lankhondo pakati pa ankhondo a Asiriya. Ndiye iwowo adayamba kuuzana kuti, “Tamvani phokosolo, mfumu ya ku Israele yalemba mafumu a Ahiti ndi a Aejipito kuti adzatithire nkhondo!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:6
21 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.


Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka mu Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu.


Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.


Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake.


Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.


M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.


Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.


Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Ejipito, kuti adzakupatsa magaleta ndi apakavalo?


Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.


Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.


Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.


Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko ao ngati mkokomo wa agaleta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.


Ndipo anaima yense m'mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, nafuula, nathawa.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa