Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.” Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:6
12 Mawu Ofanana  

Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova padziko lapansi.


Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.


Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake aamuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.


Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.


Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.


Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala.


Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu.


ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.


Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.


Koma m'mawa mwake mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa