Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:4 - Buku Lopatulika

4 Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako aamuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mukaloŵe m'nyumba mwanu, mukadzitsekere momwemo inuyo ndi ana anuwo. Ndipo mukatsanyulire mafuta m'mbiya zonsezo. Ina ikadzaza, mukaiike pambali.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:4
13 Mawu Ofanana  

Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.


Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake aamuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.


Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.


Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.


Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.


Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa