Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:9 - Buku Lopatulika

9 Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero mfumu ya ku Israele pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda kudzanso mfumu ya ku Edomu, onsewo adapita limodzi. Ndipo atayenda mozungululira m'chipululu masiku asanu ndi aŵiri, kunalibe madzi oti amwe asilikali pamodzi ndi nyama zosenza katundu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:9
16 Mawu Ofanana  

ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.


Ndipo mu Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.


Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuke, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere.


Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.


Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.


Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.


Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu.


Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.


Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.


Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi.


Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.


Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.


Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?


Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.


Nachokera ku Alusi, nayenda namanga mu Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.


Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa