Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo kunali chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, kunyumba ya Yehova, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo kunali chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, kunyumba ya Yehova, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chaka cha 18 cha ufumu wake, Yosiya adatuma Safani mwana wa Azaliya, mwana wa Mesulamu, mlembi wa ku Nyumba ya Chauta, nati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati,

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:3
7 Mawu Ofanana  

Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.


koma Paska ili analichitira Yehova mu Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.


amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.


Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.


Pamene Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, anamva m'buku mau onse a Yehova,


anatsikira kunyumba ya mfumu, nalowa m'chipinda cha mlembi; ndipo, taonani, akulu onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akulu onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa