2 Mafumu 22:4 - Buku Lopatulika4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 “Pita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti aŵerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Chauta, zimene alonda apakhomo adasonkhanitsa kwa anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. Onani mutuwo |
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.