Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:2 - Buku Lopatulika

2 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono adachita zoipa kuchimwira Chauta, komabe osalingana ndi mafumu a ku Israele amene ankalamulira, iyeyo asanaloŵe ufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:2
13 Mawu Ofanana  

Koma Omuri anachimwa pamaso pa Yehova, nachita zoipa koposa onse adamtsogolerawo.


Ndipo Ahabu mwana wa Omuri anachimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo.


Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.


Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.


Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.


Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa