Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 12:3 - Buku Lopatulika

3 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 12:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.


Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.


Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.


Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.


Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.


Anauzanso anthu okhala mu Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'chilamulo cha Yehova.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa