2 Mafumu 12:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Nthaŵi ina mfumu Yowasi adauza ansembe kuti, “Musunge bwino ndalama zonse zimene zimaperekedwa ngati zopereka zopatulika ku Nyumba ya Chauta, ndiye kuti ndalama za msonkho wa munthu aliyense, ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.