Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 11:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Atsogoleriwo adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao pa Sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao kulonda pa Sabata. Onsewo adafika kwa Yehoyada wansembe uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 11:9
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.


Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.


Selomoti amene ndi abale ake anayang'anira chuma chonse cha zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akulu a nyumba za akulu, akulu a zikwi ndi mazana, adazipatula.


Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa