Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 11:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Wansembeyo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa m'Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 11:10
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.


Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m'manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.


Natenga Davide zikopa zagolide zinali pa anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.


Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu.


Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa