Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 11:25 - Buku Lopatulika

25 Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Katatu Aroma adandimenya ndi ndodo. Kamodzi anthu adandiponya miyala. Katatu pa maulendo athu apanyanja, chombo chathu chidasweka. Nthaŵi ina ndidayandama pakati pa nyanja tsiku lathunthu, usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 11:25
12 Mawu Ofanana  

nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.


Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.


Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala,


Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.


Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.


kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.


ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika;


anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa