2 Akorinto 11:26 - Buku Lopatulika26 paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mudzi, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Pa maulendo anga ochuluka ndidakumana ndi zoopsa za mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa Ayuda anzanga, ndi zina zochokera kwa akunja. Ndidapeza zoopsa m'mizinda, m'thengo, ndi pakati pa abale onyenga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. Onani mutuwo |