Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 9:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Tsono mbandakucha Samuele adaitana Saulo padengapo kuti, “Dzuka, ndikuperekeze, ndikutule apo.” Pompo Saulo adadzuka, ndipo onse aŵiriwo adakaloŵa mu mseu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:26
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.


Atatuluka m'mzinda asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?


Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sungathe kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu.


Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pabulu; nanyamuka mwamunayo, nanka kwao.


Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.


Ndipo pamene analikutsika polekeza mzinda, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa