Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 9:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo pamene analikutsika polekeza mzinda, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Atafika kothera kwake kwa mzindawo, Samuele adauza Saulo kuti, “Uza mnyamatayu kuti abatsogola, iwe wekha uime pang'ono, kuti ndikuuze mau ochokera kwa Mulungu.” Mnyamata uja adatsogola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:27
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.


Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa