Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 9:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Choncho wophika uja adatenga mwendo wa nyama naupereka kwa Saulo. Ndipo Samuele adati, “Nayi nyama imene ndidaakusungira. Idya, chifukwa ndidaakuikira padera kuti pa nthaŵi yake ino, uidye pamodzi ndi anthu amene ndidaŵaitana.” Choncho Saulo adadya ndi Samuele tsiku limenelo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:24
6 Mawu Ofanana  

Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;


Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;


Longamo pamodzi ziwalo zake, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.


Ndipo nyama yake ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.


Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa