1 Samueli 9:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Iwo adayankha kuti, “Inde, alipo. Akunka patsogolo panupa. Fulumirani. Wangofika tsopano apa mumzindamu, chifukwa anthu akukapereka nsembe lero ku kachisi ku phiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri. Onani mutuwo |