1 Samueli 9:13 - Buku Lopatulika13 mutafika m'mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Mukangoloŵa mumzindamo, mumpeza asanapite kukachisiko kuti akadye. Anthu sangayambe kudya mpaka iye atabwera, poti ayenera kuyamba waidalitsa nsembeyo. Pambuyo pake ndiye anthu oitanidwa adzayamba kudya. Tsono pitani, mukumana naye posachedwa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.” Onani mutuwo |