Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Pambuyo pake Davide adakafika kwa anthu 200 otopa kwambiri ndi osathanso kuyenda aja, amene adaaŵasiya ku mtsinje wa Besori. Iwo adanyamuka napita kukakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye aja. Davide adaŵayandikira naŵalonjera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:21
7 Mawu Ofanana  

Chikondi cha pa abale chikhalebe.


Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;


Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?


nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao.


Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.


Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.


Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuke nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa