Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Adalanditsanso nkhosa zonse ndi ng'ombe zomwe. Ndipo anthu ankakusa zoŵetazo namati, “Izi ndi za Davide.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:20
7 Mawu Ofanana  

Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.


Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.


Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa