Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:22 - Buku Lopatulika

22 Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuke nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pamenepo anthu ena oipa mtima ndi opandapake a m'gulu la amene adaapita ndi Davide aja, adati, “Chifukwa chakuti sadapite nafe, sitiŵapatsako zofunkha zimene talanditsazi, kungopatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake, ndipo achoke.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:22
10 Mawu Ofanana  

ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.


Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mzinda, namponya miyala, namupha.


Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.


Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;


Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mzindawo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.


Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaone anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.


Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.


Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa