Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 29:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Apo Akisi adaitana Davide namuuza kuti, “Pali Chauta wamoyo, iwe wakhala wokhulupirika kwa ine, ndipo kutumikira kwako m'magulu anga ankhondo kwandikomera kwambiri. Sindidakupeze cholakwa kuyambira tsiku limene udabwera kuno mpaka lero lino. Komabe atsogoleri enaŵa sakukufuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kotero Akisi anayitana Davide ndipo anamuwuza kuti, “Pali Yehova wamoyo, iwe wakhala wodalirika ndipo chikanakhala chinthu chabwino kuti uzimenya nkhondo pamodzi nane popeza chibwerere iwe kuno ine sindinapeze cholakwa chilichonse ndi iwe. Koma atsogoleri enawa ndiwo sakukufuna.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 29:6
19 Mawu Ofanana  

Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.


Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.


Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.


Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako.


chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.


Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.


wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.


Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.


Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.


Chifukwa chake, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti.


Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa