Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 28:23 - Buku Lopatulika

23 Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Saulo adakana nati, “Ine sindidya ai.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo adamkakamiza, ndipo adaŵamvera. Choncho adadzuka pansi paja nakhala pa bedi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iye anakana ndipo anati, “Ayi, ine sindidya.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo anamuwumiriza, ndipo anawamvera. Choncho anadzuka pansi nakhala pa bedi.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 28:23
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.


Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.


Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?


panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.


Monga wovula malaya tsiku lamphepo, ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.


ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pake; pamenepo unaika chofukiza chonga ndi mafuta anga.


Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.


Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao.


Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.


Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;


Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa