Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:10 - Buku Lopatulika

10 Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Makono ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nabala adayankha anyamata a Davide aja poŵafunsa kuti, “Kodi Davide mwana wa Yese ndani? Ha! Masiku ano pali anthu antchito ambiri amene akuthaŵa kwa ambuyao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Nabala anayankha anyamata a Davide kuti, “Kodi Davide ndi ndani? Mwana wa Yese ndi ndani? Masiku ano pali antchito ambiri amene akuthawa kwa mabwana awo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.


Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.


Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.


Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.


Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.


Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?


Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa