Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:11 - Buku Lopatulika

11 Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Kodi ndingatenge chakudya changa, madzi anga, nyama yanga imene ndaphera anyamata anga ometa nkhosa, kuti ndipatse anthu omwe sindikudziŵa kumene akuchokera?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nditengerenji buledi, madzi ndi nyama zimene ndaphera anthu anga ometa nkhosa ndi kuzipereka kwa anthu amene sindikudziwa kumene achokera?”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:11
16 Mawu Ofanana  

kapena kudya nthongo yanga ndekha, osadyako mwana wamasiye;


monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;


Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.


ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?


Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?


Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.


Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.


Chomwecho anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.


Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.


Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa