Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Saulo adadzera mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake adadzeranso mbali ina ya phirilo. Tsono Davide ndi anthu ake adafulumira kuthaŵa, pamene Saulo ndi anthu ake anali pafupi kuŵagwira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Sauli amayenda mbali ina ya phirilo, ndipo Davide ndi anthu ake nawonso anali mbali ina ya phirilo. Koma Davide ndi anthu ake anafulumira kumuthawa Sauli pamene Sauliyo ndi anthu ake ali pafupi kuwagwira.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:26
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.


Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.


Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu, apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.


kundilanditsa kwa oipa amene andipasula, adani a pa moyo wanga amene andizinga.


Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga; mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.


Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.


Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;


Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mzinda wokondedwawo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa.


Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.


Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.


Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.


Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni.


Koma mthenga unafika kwa Saulo ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yovumbulukira ya Afilisti yalowa m'dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa