Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:10 - Buku Lopatulika

10 Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mzindawo chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono Davide adalankhula ndi Mulungu kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndithudi, ine mtumiki wanu ndamva kuti Saulo akufunafuna kubwera kuno ku Keila, kuti adzaononge mzindawu chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono Davide anayankhula ndi Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, ine mtumiki wanu ndamva ndithu kuti Sauli akufuna kubwera ku Keila ndi kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:10
8 Mawu Ofanana  

Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?


Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.


Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.


Ndipo anakantha Nobu ndiwo mzinda wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.


Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.


Ndipo Saulo anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ake.


Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa