1 Samueli 20:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe. Onani mutuwo |