Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 19:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 pompo adatumanso anthu kuti akamgwire. Anthuwo adaona gulu la aneneri akuvina namalosa, Samuele akuŵatsogolera. Pamenepo mzimu wa Mulungu udaŵaloŵa anthuwo ndipo nawonso adayamba kulosa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 19:20
13 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;


Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.


Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.


Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.


Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao.


Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.


Ndipo pamene Saulo anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, Iye alikudwala.


Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti mu Rama.


Ndipo pamene anauza Saulo, iye anatumiza mithenga ina; koma iyonso inanenera. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kachitatu, nayonso inanenera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa