Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 18:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Davide adanyamuka napita pamodzi ndi ankhondo ake, ndipo adakapha Afilisti 200. Adabwera nato timakungu tija natipereka kwa mfumu, kuti choncho akhale mkamwini wake. Apo Saulo adapatsa Davideyo mwana wake Mikala, kuti akhale mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 18:27
8 Mawu Ofanana  

Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.


Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.


Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.


Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;


Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.


Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.


Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide.


Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa