Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 18:25 - Buku Lopatulika

25 Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Tsono Saulo adati, “Kamuuzeni kuti, sindikufuna chiwongo cha mtundu uliwonse ai, ndingofuna timakungu ta nsonga za mavalo a Afilisti 100, kuti ndilipsire adani anga.” Potero Saulo ankaganiza zoti Davide aphedwe ndi Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’ ” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 18:25
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.


Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.


Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.


Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti.


Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.


Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide.


Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa