Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 17:42 - Buku Lopatulika

42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 17:42
9 Mawu Ofanana  

Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo.


Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.


Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.


Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.


Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa