1 Samueli 17:40 - Buku Lopatulika40 Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201440 Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa40 Tsono adatenga ndodo yake m'manja. Adatola miyala isanu yosalala yakumtsinje, naiika m'thumba lake lakubusa. Ali ndi khwenengwe m'manja, adapita kukakumana ndi Mfilisti uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero40 Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja. Onani mutuwo |