1 Samueli 17:39 - Buku Lopatulika39 Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201439 Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazivula Davide. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa39 Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero39 Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere. Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula. Onani mutuwo |