1 Samueli 17:28 - Buku Lopatulika28 Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Eliyabu, mkulu wake, atamva Davideyo akulankhula ndi anthu, adamupsera mtima, namufunsa kuti, “Wadzachita chiyani kuno? Nanga nkhosa zija wasiyira yani ku chipululu? Ndikudziŵa kuti ndiwe wodzikuza ndi woipa mtima. Wadza kuno kudzangoona nkhondo chabe!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Eliabu, mkulu wake wa Davide, atamumva akuyankhula ndi anthuwo, anamukwiyira ndipo anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabwera kuno? Ndipo wasiyira yani nkhosa zochepazo mʼchipululu? Ndikudziwa kuti ndiwe wodzikuza ndiponso woyipa mtima. Unabwera kuno kuti udzaonere nkhondo.” Onani mutuwo |