Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 16:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Uitane Yese kunsembeko, tsono Ine ndikakulangiza zoti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakutchulire.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ukamuyitane Yese ku mwambo wa nsembe, ndipo ine ndidzakuwuza choti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakulozere.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 16:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.


Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.


Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.


komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.


Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa