1 Samueli 14:36 - Buku Lopatulika36 Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Mulungu kuno. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201436 Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa36 Pamenepo Saulo adati, “Tiyeni tipite usiku, tilondole Afilisti, ndipo tilande zinthu zao mpaka m'maŵa kutacha. Tisasiyepo ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Anthuwo adati, “Chitani chilichonse chimene chikukukomerani.” Koma wansembe adati, “Tiyeni tiyambe tapempha nzeru kwa Mulungu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero36 Sauli anati, “Tiyeni titsatire Afilisti usikuwu ndi kulanda zinthu zawo mpaka mmawa. Tisasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.” Ankhondowo anayankha kuti, “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.” Koma wansembe anati, “Tipemphe uphungu kwa Mulungu poyamba.” Onani mutuwo |