Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

1 Samueli 14:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Ndipo adatinso, “Mwazikanani pakati pa anthu, muŵauze kuti, ‘Aliyense abwere ndi ng'ombe yake, kapena nkhosa yake, aziphere pompano, kenaka adye. Ndipo musachimwire Chauta podyera kumodzi ndi magazi.’ ” Motero aliyense mwa anthuwo adabwera ndi ng'ombe yake usiku umenewo, naiphera komweko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Kenaka Sauli anati, “Mwazikanani pakati pa anthu ndi kukawawuza kuti aliyense abwere ndi ngʼombe yake kapena nkhosa yake, ndipo adzayiphe pomwe pano ndi kuyidya. Musachimwire Yehova pakudya nyama imene ili ndi magazi.” Kotero aliyense anabwera ndi ngʼombe yake usiku womwewo ndi kuyipha pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

1 Samueli 14:34
3 Mawu Ofanana  

Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

Pamenepo anauza Saulo, kuti, Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munachita konyenga; kunkhunizani mwala waukulu kwa ine lero.

Ndipo Saulo anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.

Titsatireni:

Zotsatsa

Zotsatsa