2 Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.

2 Ana a Tola naŵa: Uzi, Refaya, Yeriyele, Yamai, Ibisamu, ndi Semuele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ndiye kuti a banja la Tola. Onsewo anali ankhondo amphamvu pa mibadwo yao. Chiŵerengero chao pa nthaŵi ya Davide chinali 22,600.
2 Ana a Tola ndi awa: Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.