Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 8:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya mu Kachisi wa fano, kodi chikumbumtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m'Kachisi wa fano, kodi chikumbu mtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ngati iweyo amene uli wodziŵa udya m'nyumba yopembedzeramo fano, nanga tsono munthu wosadziŵa kwenikweni, atakuwona ukuchita zimenezi, kodi chimenechi sichidzamlimbitsa mtima kuti nayenso azidya chakudya choperekedwa kwa mafano?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano?

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 8:10
13 Mawu Ofanana  

nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.


popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.


koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.


Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.


Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo.


Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;


Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.


Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.


Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo.


Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa