Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 5:13 - Buku Lopatulika

13 koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mulungu adzaweruza akunja. “Chotsani woyipayo pakati panu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 5:13
18 Mawu Ofanana  

Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.


Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.


Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.


chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.


tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.


kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;


Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.


Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.


Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse. Potero muzichotsa choipacho pakati panu.


Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.


muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala mu Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa