Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 6:1 - Buku Lopatulika

1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ngati wina ali ndi mlandu ndi mkhristu mnzake, angathe bwanji kukauzengetsa kwa oweruza amene ali akunja, osati kwa akhristu anzake?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pamene wina wa inu ali ndi mlandu ndi mnzake, nʼchifukwa chiyani amatengera nkhaniyo kwa anthu akunja kuti akawaweruze mʼmalo mopita nayo kwa oyera mtima?

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 6:1
11 Mawu Ofanana  

kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.


Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane.


kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.


Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),


Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruze ndi inu,


Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa