Zefaniya 2:4 - Buku Lopatulika Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mzinda wa Gaza udzasiyidwa, Asikeloni adzasanduka bwinja. Anthu a ku Asidodi adzapirikitsidwa masana mwadzidzidzi, Akeroni adzapasuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gaza adzasiyidwa ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja. Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu ndipo Ekroni adzazulidwa. |
Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.
Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.
ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,
Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka.