Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yuda 1:13 - Buku Lopatulika

mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ali ngati mafunde aukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zao. Ali ngati nyenyezi zosokera, ndipo Mulungu akuŵasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya. Mbiri iyi idadziŵika pakati pa Aisraele, koma siinalembedwe m'Chipangano Chakale.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.

Onani mutuwo



Yuda 1:13
12 Mawu Ofanana  

Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ake, ndi phokoso la mitundu ya anthu.


Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi uve.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.


Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.


Angelonso amene sanasunge chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.


Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.