Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Yohane 7:2 - Buku Lopatulika Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵiyo nkuti chikondwerero cha Misasa chili pafupi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, |
Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.
Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;