Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 8:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu Solomoni nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Mfumu Solomoni nthawi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 8:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.


Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.


Ndipo amuna onse a Israele anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anachitikawo, m'mwezi wachisanu ndi chiwiri.


Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;


Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.


Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.


Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.


Mudzichitire chikondwerero cha Misasa masiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa