Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.
Obadiya 1:16 - Buku Lopatulika Pakuti monga munamwa paphiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe unamwa pa phiri langa loyera, koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza; iwo adzamwa ndi kudzandira ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi. |
Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.
Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.
kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.
Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,
Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga.
Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?