Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Numeri 9:7 - Buku Lopatulika nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?” |
Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake.